Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 16:5 - Buku Lopatulika

5 Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukachita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndachotsa mtendere wanga pa anthu awa, chifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukachita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndachotsa mtendere wanga pa anthu awa, chifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Chauta akunena kuti, “Usaloŵe m'nyumba ya maliro. Usaloŵemo kuti ukalire kapena kutonthoza anthu, pakuti ndaŵachotsera mtendere wanga. Ndachotsanso chikondi changa chosasinthika ndiponso chifundo changa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yehova akuti, “Usalowe mʼnyumba ya maliro; usapite kukalira maliro kapena kukapepesa, chifukwa Ine ndawachotsera madalitso anga, chikondi changa ndi chifundo changa.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 16:5
13 Mawu Ofanana  

Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu; pakuti izi nza kale lonse.


Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


Akufunkha afika pa mapiri oti see m'chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.


Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawaononge.


chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.


Watalikitsanso moyo wanga ndi mtendere; ndinaiwala zabwino.


Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.


Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?


Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa