Yeremiya 15:9 - Buku Lopatulika9 Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lake lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lake lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Mai wa ana asanu ndi aŵiri wakomoka, akupuma mwabefu. Mdima wamgwera kukadali masana. Adamchititsa manyazi ndipo wataya mtima. Otsala onse ndidzaŵapereka kwa adani kuti aŵaphe ndi lupanga,” akuterotu Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka ndipo akupuma wefuwefu. Dzuwa lake lalowa ukanali usana; anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru. Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo kuti awaphe ndi lupanga,” akutero Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.