Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 15:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita mu Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita m'Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndidzaŵasandutsa chinthu chochititsa nyansi kwa anthu a m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, adachita ku Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 15:4
19 Mawu Ofanana  

Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba.


popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao mu Ejipito, mpaka lero lino.


Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.


Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu zisanu.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawachotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israele.


Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.


Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;


Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvere Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kumliri, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.


Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwe; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.


Yerusalemu wachimwa kwambiri; chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa; onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche; inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.


Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wake? Mwanayo akachita chiweruzo ndi chilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwachita, adzakhala ndi moyo ndithu.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzawakweretsera msonkhano wa anthu, ndi kuwapereka awazunze, ndi kulanda chuma chao.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa