Yeremiya 15:5 - Buku Lopatulika5 Pakuti ndani adzakuchitira iwe chisoni, Yerusalemu? Ndani adzakulirira iwe? Ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Pakuti ndani adzakuchitira iwe chisoni, Yerusalemu? Ndani adzakulirira iwe? Ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Chauta akuti, “Kodi inu a ku Yerusalemu adzakumverani chisoni ndani? Adzakulirani ndani? Ndani adzapatuke kuti akufunseni za moyo wanu? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 “Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu? Kodi adzakulira ndani? Kodi ndani amene adzapatuka kufunsa za moyo wako? Onani mutuwo |
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.