Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 15:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Ndidzaŵagwetsera zinthu zinai izi zoŵaononga: lupanga loŵapha, agalu oŵaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zilombo zoti ziŵaphe ndi kuŵadya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 15:3
21 Mawu Ofanana  

kuti uviike phazi lako m'mwazi, kuti malilime a agalu ako alaweko adani ako.


Adzasiyira mbalame zakulusa za m'mapiri ndi zilombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m'dzinja, ndi zilombo zonse za dziko zidzakhalapo m'malimwe.


Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m'thengo, mudze nazo zidye.


Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.


Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.


Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.


Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zilombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa.


Wapambutsa njira zanga, nanding'amba; nandipululutsa.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?


Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zilombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.


ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.


Popeza ndidzatumiza chilombo chakuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu ndipo chidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.


Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'mizinda mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.


Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka.


Ndipo mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zilombo zonse za padziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa.


Adzaonda nayo njala adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa; ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo, ndi ululu wa zokwawa m'fumbi.


Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa