Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 15:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Akakufunsa kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ Uŵauze kuti Ine ndati, “ ‘Oyenera mliri adzafa ndi mliri, oyenera lupanga adzafa ndi lupanga, oyenera njala adzafa ndi njala, oyenera ukapolo, adzapita ku ukapolo.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti, “ ‘Oyenera kufa adzafa; oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga; oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala; oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 15:2
18 Mawu Ofanana  

Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.


Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.


Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.


Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.


Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi padzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m'mlengalenga, ndi cha zilombo za dziko lapansi.


Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Ejipito; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.


Uziti, Ine ndine chizindikiro chanu, monga ndachita ine momwemo kudzachitidwa nao; adzachotsedwa kunka kundende.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?


Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zilombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.


Ndipo anakwaniritsa mau ake adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera choipa chachikulu; pakuti pansi pa thambo lonse sipanachitike monga umo panachitikira Yerusalemu.


Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka.


Pamenepo ndinati, Sindidzadyetsanso inu; chilikufa chife; chosoweka chisoweke; ndi zotsala zidyane, chonse nyama ya chinzake.


Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa