Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 11:5 - Buku Lopatulika

5 kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko moyenda mkaka ndi uchi, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko moyenda mkaka ndi uchi, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Choncho ndidzachita zimene ndidalonjeza makolo anu molumbira, zakuti ndidzaŵapatsa dziko lamwanaalirenji, dziko limene mukukhalamoli.’ ” Tsono ine ndidayankha kuti, “Zikhale momwemo, Inu Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Tsono Ine ndidzakwaniritsa lumbiro lomwe ndinalumbira kwa makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,’ dziko lomwe inu lero mukukhalamo.” Tsono Ine ndinayankha kuti, “Ameni, Yehova.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:5
16 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, achitike mau anu amene munanena kwa Davide mtumiki wanu.


Akumbukira chipangano chake kosatha, mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;


Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.


Ndidzatero ndi malo ano, ati Yehova, ndi okhalamo, kusanduliza mzinda uwu ngati Tofeti;


Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am'nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno.


ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uchi;


Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu.


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?


Potero imvani, Israele, musamalire kuwachita, kuti chikukomereni ndi kuti muchuluke chichulukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa