Yeremiya 11:4 - Buku Lopatulika4 limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, m'ng'anjo ya chitsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, m'ng'anjo ya chitsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 chimene ndidachita ndi makolo anu, nditaŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Nditaŵachotsa m'ng'anjo ya moto ija, ndidati, ‘Mukamandimvera ndi kumachita zimene ndikuuzani, inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Awa anali mawu amene ndinalamulira makolo anu nditawatulutsa mu Igupto, kuchoka mʼngʼanjo yamoto.’ Ine ndinati, ‘Mverani Ine ndi kuchita chilichonse chimene ndakulamulirani. Mukatero mudzakhala anthu anga ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Onani mutuwo |