Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 11:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau onsewa m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwachita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau aonsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwachita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Ulalike mau onseŵa ku mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Uŵauze kuti, ‘Imvani mau a chipangano ichi, ndipo muŵasunge.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova anandiwuza kuti, “Lengeza mawu onsewa mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu: ‘Mverani mawu a pangano ili ndi kuzitsatira.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:6
13 Mawu Ofanana  

Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.


Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.


nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la Chipata cha Mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;


Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo.


Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse.


Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.


Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'mizinda mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo?


Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.


pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.


Ndipo tsopano, Israele, tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwachite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.


Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati padziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu.


Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa