Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 1:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pake unafulatira kumpoto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pake unafulatira kumpoto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Chauta adandifunsa kachiŵiri kuti, “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona mbiya yogaduka, yafulatira kumpoto.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona mʼphika wa madzi owira, ndipo wagudukira kuno kummwera.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 1:13
10 Mawu Ofanana  

Ndipo lotolo linabwerezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita.


momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona chiyani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa.


ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mzinda uwu ndi mphika, ife ndife nyama.


Chifukwa chake atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwake, iwo ndiwo nyama imene, ndi mzinda uwu ndiwo mphika; koma inu mudzatulutsidwa m'kati mwake.


Chifukwa chake uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzachitika, ati Ambuye Yehova.


Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso.


Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikaponyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa