Rute 4:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Nthaŵi yomweyo Bowazi adapita ku chipata cha mzinda nakakhala pansi, pa bwalo losonkhanirana. Tsono adangoona wachibale ankanena uja akufika. Apo Bowazi adati, “Bwenzi langa, tapatukira kuno, ukhale pansi apa.” Munthu uja adapatuka nakhala pansi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Nthawi yomweyo Bowazi anapita ku chipata cha mzinda ndi kukhala pansi kumeneko pabwalo losonkhanira. Tsono anangoona wachibale woyenera kulowa chokolo uja akufika. Ndipo Bowazi anati, “Patukirani kuno, bwenzi langa. Mubwere mudzakhale apa.” Choncho anapatuka nakakhala pansi. Onani mutuwo |