Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 3:10 - Buku Lopatulika

10 Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsate anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Apo Bowazi adati, “Chauta akudalitse, mwana wanga. Zabwino wachita potsirizazi zikupambana zoyamba zija zimene udachitira mpongozi wako, poti sudapite kwa anyamata osauka kapena olemera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndipo Bowazi anati, “Mwana wanga, Yehova akudalitse popeza kukoma mtima kumene wasonyeza panoku kwaposa koyamba kaja. Iwe sunathamangire anyamata olemera kapena osauka.

Onani mutuwo Koperani




Rute 3:10
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.


Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.


Ndipo Bowazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi amai ako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.


Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.


Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.


Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mufunde mdzakazi wanu chofunda chanu, pakuti inu ndinu wondiombolera cholowa.


Ndipo Samuele anadza kwa Saulo; ndipo Saulo anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinachita lamulo la Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa