Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 2:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo mnyamata woyang'anira ochekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmowabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Mowabu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo mnyamata woyang'anira ochekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmowabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Mowabu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Kapitao wakeyo adayankha kuti, “Maiyu ndi Mmowabu amene adabwera ndi Naomi kuchokera ku dziko la Mowabu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kapitawo uja anayankha kuti, “Mayiyu ndi Mmowabu amene anabwera ndi Naomi kuchokera ku dziko la Mowabu.

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:6
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko?


Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga:


Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, naika m'manja mwake zonse anali nazo.


Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba.


Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?


Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga;


Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?


Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.


Nati Bowazi kwa mnyamata woyang'anira ochekawo, Mkazi uyu ngwa yani?


ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa