Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 2:7 - Buku Lopatulika

7 ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Iyeyu wandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkheko barele m'munda m'mene anthu akolola kale!’ Choncho wakhala akukunkha kuyambira m'mamaŵa mpaka tsopano lino, osapuma ndi pang'ono pomwe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iye anandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkhe barele mʼminda moti akololamo kale.’ Iye wakhala akukunkha kuyambira mmawa mpaka tsopano lino osapuma nʼpangʼono pomwe.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:7
14 Mawu Ofanana  

Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu; koma moyo wa akhama udzalemera.


Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.


Wosauka amadandaulira; koma wolemera ayankha mwaukali.


Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.


musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye;


Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.


ndi kumverana wina ndi mnzake m'kuopa Khristu.


Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.


Ndipo Rute Mmowabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kucheka zanga zonse za m'minda.


Ndipo mnyamata woyang'anira ochekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmowabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Mowabu;


Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa