Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Oweruza 1:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamenepo Ayuda adauza abale ao, anthu a fuko la Simeoni, kuti, “Tiyeni tipite limodzi m'dziko limene Chauta adagaŵira ife, kuti tikamenyane ndi Akanani. Pambuyo pake nafenso tidzapita nanu limodzi m'dziko limene adagaŵira inu.” Choncho Asimeoni adatsakana nawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Choncho Ayuda anawuza abale awo a fuko la Simeoni kuti, “Bwerani tipitire limodzi mʼdziko limene tapatsidwa kuti tikamenyane ndi Akanaani. Ifenso tidzapita nanu mʼdziko limene anakugawirani.” Ndipo Asimeoni anapita nawo.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 1:3
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Chifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamutcha dzina lake Simeoni.


Ndipo iye anati, Aaramu akandipambana ine, udzandithandiza ndiwe, koma ana a Amoni akapambana iwe, tsono ndidzabwera ine kukuthandiza.


Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.


Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.


Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkulu wake, nakantha Akanani akukhala mu Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mzindawo analitcha Horoma.


Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m'dzanja lake.


Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa