Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Obadiya 1:16 - Buku Lopatulika

16 Pakuti monga munamwa paphiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Anthu anga adamwa chikho cha zoŵaŵa pa phiri langa loyera, koma mitundu ina ya anthu idzamwa chikho cha zoŵaŵa kopitirira. Idzachita kugugudiza chikhocho kenaka nkuzimirira pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Iwe unamwa pa phiri langa loyera, koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza; iwo adzamwa ndi kudzandira ndipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:16
13 Mawu Ofanana  

Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.


Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwe kuti amwe chikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? Sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.


kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dziko la Uzi; chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kuvula zako.


Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,


Adzera chiwawa onsewo; nkhope zao zikhazikika zolunjika m'tsogolo; asonkhanitsa andende ngati mchenga.


Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa