Numeri 7:19 - Buku Lopatulika19 anabwera nacho chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 anabwera nacho chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Zopereka zake zinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Chopereka chomwe anabwera nacho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, molingana ndi muyeso wa ku malo opatulika. Mbale zonse zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha chakudya. Onani mutuwo |