Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 7:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka chiperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera nacho chopereka chao paguwa la nsembelo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka chiperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera nacho chopereka chao pa guwa la nsembelo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pambuyo pake atsogoleri adabwera ndi zopereka zopatulira guwa pa tsiku lomwe adalidzozalo. Ndipo adafika nazo zopereka zao patsogolo pa guwalo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Guwa la nsembe litadzozedwa, atsogoleri anabweretsa zopereka zawo zopatulira guwa nazipereka paguwapo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 7:10
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova.


Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ya ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Mulungu.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu anachita msonkhano woletsa; popeza anachita zakupereka guwa la nsembe masiku asanu ndi awiri, ndi madyerero masiku asanu ndi awiri.


Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti achite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.


Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi chimwemwe chachikulu; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi chikondwerero cha Yerusalemu chinamveka kutali.


Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa, ndipo simunandikondwetsere adani anga.


Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Akalonga onse, yense pa tsiku lake, apereke zopereka zao za kupereka chiperekere guwa la nsembe.


Uku ndi kupereka chiperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israele, tsiku la kudzoza kwake: mbale zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolide khumi ndi ziwiri;


ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.


Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa