Numeri 6:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 mwiniwakeyo akhale wake wa Chauta masiku onse a kudzipereka kwake. Tsono abwere ndi mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti aperekere nsembe yopepesera kupalamula. Koma masiku a kudzipereka kwake koyamba kuja asaŵerengere, chifukwa kudzipereka kwakeko adakuipitsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake. Onani mutuwo |
Koma wolungamayo akabwerera kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, ndi kuchita monga mwa zonyansa zonse azichita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena chimodzi cha zolungama zake zonse adzazichita chidzakumbukika m'kulakwa kwake analakwa nako, ndi m'kuchimwa kwake anachimwa nako; momwemo adzafa.