Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 6:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 mwiniwakeyo akhale wake wa Chauta masiku onse a kudzipereka kwake. Tsono abwere ndi mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti aperekere nsembe yopepesera kupalamula. Koma masiku a kudzipereka kwake koyamba kuja asaŵerengere, chifukwa kudzipereka kwakeko adakuipitsa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:12
12 Mawu Ofanana  

Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi.


“ ‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.


Wansembe atenge mwana wankhosa wopereka nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule kuti zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


Pambuyo pake, munthuyo abwere kwa Yehova ndi mwana wankhosa wamkazi kapena mbuzi kuti ikhale chopereka chopepesera tchimo ndipo wansembe achite mwambo wopepesera tchimo lomwe wachitalo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo.


“ ‘Ngati munthuyo alibe mwana wankhosa, abweretse njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri kwa Yehova ngati chopereka chopepesera tchimo lake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera tchimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.


Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake.


“Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano.


koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka.


Yesu anayankha kuti, “Zibatero tsopano, ndi koyenera kwa ife kuchita zimenezi kukwaniritsa chilungamo chonse.” Ndipo Yohane anavomera.


Pakuti amene amasunga Malamulo onse, akangophwanya fundo imodzi yokha, waphwanya Malamulo onse.


Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma chitani khama kuti mukalandire mphotho yanu yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa