Numeri 5:27 - Buku Lopatulika27 Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nachita mosakhulupirika pa mwamuna wake, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa thupi lake, ndi m'chuuno mwake mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nachita mosakhulupirika pa mwamuna wake, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa thupi lake, ndi m'chuuno mwake mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Mkazi atamwa madziwo, akakhala kuti adadziipitsa, kapena sadakhale wokhulupirika kwa mwamuna wake, madzi amatemberero aja adzaloŵa m'mimba mwake, ndipo iyeyo adzamva ululu woopsa. Thupi lake lidzatupa, m'chiwuno mwake mudzafwapa, ndipo mkaziyo adzakhala wotembereredwa pakati pa anthu a mtundu wake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Ndipo ngati mkaziyo anadzidetsadi ndi kukhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, pamene amwa madzi obweretsa matemberero aja, nalowa mʼmimba mwake, adzamva ululu woopsa. Mimba yake idzatupa ndi ntchafu yake idzawonongeka ndipo adzakhala wotembereredwa pakati pa anthu ake. Onani mutuwo |
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.
Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.