Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 5:26 - Buku Lopatulika

26 Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, chikumbutso chake, nachitenthe paguwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, chikumbutso chake, nachitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Wansembe atapeko ufa wa dzanja limodzi kuti ukhale chikumbutso ndi kuutenthera pa guwa. Pambuyo pake apatse mkaziyo madzi aja kuti amwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Tsono wansembeyo atapeko ufa dzanja limodzi kuti ukhale wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa lansembe. Atatha izi, amwetse mkaziyo madzi aja.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:26
5 Mawu Ofanana  

Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake paguwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe paguwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo adze nacho kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale chikumbutso chake, nachitenthe paguwa la nsembe monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.


Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa chopereka cha ufa wosalala, ndi pa mafuta ake, ndi lubani lonse lili pa chopereka chaufa, nazitenthe paguwa la nsembe, zichite fungo lokoma, ndizo chikumbutso chake cha kwa Yehova.


Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa yansanje m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa