Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 5:25 - Buku Lopatulika

25 Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa yansanje m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa yansanje m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Apo wansembe achotse m'manja mwa mkaziyo chopereka cha chakudya choperekera nsanje ija. Aipereke moweyula pamaso pa Chauta, ndipo abwere nayo ku guwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Wansembe achotse mʼmanja mwa mkaziyo nsembe yachakudya ya nsanje ija, nayiweyula pamaso pa Yehova ndi kuyipereka pa guwa lansembe.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:25
6 Mawu Ofanana  

ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ake aamuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.


pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.


Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.


Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.


Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, chikumbutso chake, nachitenthe paguwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa