Numeri 36:7 - Buku Lopatulika7 Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko; popeza ana a Israele adzamamatira yense ku cholowa cha fuko la makolo ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko; popeza ana a Israele adzamamatira yense ku cholowa cha fuko la makolo ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Choloŵa cha Aisraele chisachotsedwe m'fuko lina nkuchipatsa fuko lina. Pakuti Mwisraele aliyense ayenera kukangamira pa choloŵa cha fuko la makolo ake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 kuti cholowa cha Israeli chisapite ku fuko lina, pakuti Mwisraeli aliyense ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake. Onani mutuwo |
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.