Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 36:12 - Buku Lopatulika

12 Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m'fuko la banja la atate wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m'fuko la banja la atate wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Adakwatiwa ndi a m'mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe, ndipo choloŵa chao chidakhalabe m'fuko la bambo wao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anakwatiwa mʼmafuko a zidzukulu za Manase mwana wa Yosefe, ndipo cholowa chawo chinakhalabe mʼfuko la abambo awo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 36:12
4 Mawu Ofanana  

popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana aamuna a abale a atate wao.


Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israele ndi dzanja la Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko.


Cholamulira Yehova za ana aakazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha.


Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa