Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 35:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo midzi ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Mizinda imene mudzapatse Aleviyo idzakhale mizinda isanu ndi umodzi yothaŵirako, kumene muzidzalola kuti munthu wopha mnzake mwangozi athaŵireko. Ndipo mudzaŵapatsenso mizinda ina 42, kuwonjezera pa mizinda imeneyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Isanu ndi umodzi mwa midzi imene mudzapereke kwa Alevi idzakhala mizinda yopulumukirako, kumene munthu wopha mnzake adzathawireko. Ndipo mudzawapatsenso midzi ina 42.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:6
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso;


Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikirani pothawirapo iye.


Ndipo padzakhala chihema cha mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo.


Ndipo muyese kunja kwa mzinda, mbali ya kum'mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwera mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mzindawo pakati; ndiwo mabusa a kumizinda.


Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.


kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;


Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzake, ndi Libina ndi mabusa ake;


Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Gezere ndi mabusa ake;


Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa hafu la fuko la Manase, Golani mu Basani ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; mizinda iwiri.


Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi, kutapa pa cholowa chao, monga mwa lamulo la Yehova, mizinda iyi ndi mabusa ao.


Ndipo motapira pa fuko la Nafutali, Kedesi mu Galileya ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Hamotidori ndi mabusa ake, ndi Karitani ndi mabusa ake, mizinda itatu.


Ndipo motapira pa fuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake,


Ndipo motapira m'fuko la Gadi, Ramoti mu Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa