Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 35:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo muyese kunja kwa mzinda, mbali ya kum'mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwera mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mzindawo pakati; ndiwo mabusa a kumizinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo muyese kunja kwa mudzi, mbali ya kum'mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwera mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mudziwo pakati; ndiwo mabusa a kumidzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Uyese kunja kwa mzindawo, kuvuma mamita 900, kumwera mamita 900, kuzambwe mamita 900, kumpoto mamita 900, ndipo mzindawo ukhale pakati. Dziko limeneli lidzakhala busa la mizinda yaoyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kunja kwa mudzi yezani mamita 900 kummawa, mamita 900 kumpoto ndipo mudziwo ukhale pakati. Adzakhala ndi dera limeneli ngati malo a midziyo, owetera ziweto zawo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:5
3 Mawu Ofanana  

Ndipo mabusa a mizindayo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono chikwi chimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.


Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.


Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina mu Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa