Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 35:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo mizindayo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mizindayo idzakhala malo obisalamo pothaŵa munthu wofuna kubwezera choipa, kuti munthu wopha mnzake mwangoziyo asaphedwe, mpaka akaime pamaso pa mpingo kuti umuweruze.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Adzakhala malo obisalako pothawa munthu wofuna kulipsira, kuti munthu wopha mnzake mwangozi asaphedwe mpaka akayime pamaso pa gulu la anthu kuti akaweruzidwe.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:12
10 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.


Ndipo mizindayo muipereke ikukhalireni mizinda isanu ndi umodzi yopulumukirako.


Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.


Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzake wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzake osati dala, osamuda kale lonse;


kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzake, pokhala mtima wake watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanapalamule imfa, poona sanamude kale lonse.


Nena ndi ana a Israele ndi kuti, Mudziikire mizinda yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose.


Iyi ndi mizinda yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa