Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 35:11 - Buku Lopatulika

11 muikire mizinda ikukhalireni mizinda yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 mupatule mizinda ina kuti ikhale mizinda yanu yothaŵirako, kumene munthu wopha mnzake mwangozi azithaŵirako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 sankhani midzi ina kuti ikhale mizinda yanu yopulumukirako, kumene munthu wopha munthu wina mwangozi angathawireko.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:11
9 Mawu Ofanana  

Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikirani pothawirapo iye.


Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;


Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;


Mizinda isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko.


Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo mizinda ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri.


kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wake dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa mizinda iyi, akhale ndi moyo:


Nena ndi ana a Israele ndi kuti, Mudziikire mizinda yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa