Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 32:27 - Buku Lopatulika

27 koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Koma atumiki anufe, tiwoloka aliyense atatenga zida, kukamenya nkhondo pamaso pa Chauta, monga momwe inu mbuyathu mwalamulira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 koma antchito anufe, mwamuna aliyense amene ali ndi chida cha nkhondo, adzawoloka kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova monga mbuye wathu wanenera.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 32:27
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.


Ndipo Aroni anati kwa Mose, Mfumu yanga, musatiikiretu kuchimwa kumene tapusa nako, ndi kuchimwa nako.


koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala mizinda ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo.


Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a makolo a mafuko a ana a Israele za iwo.


nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake aakazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu.


Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa