Numeri 3:36 - Buku Lopatulika36 Ndipo choyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a chihema, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake, ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito zake zonse; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201436 Ndipo choyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake, ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito zake zonse; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa36 Ntchito imene ana aamuna a Merari adapatsidwa, inali yosamala mitengo ya malo opatulika monga: nsichi zake, mizati yake, masinde ake ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Ankayang'anira ntchito zonse zokhudza zimenezi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero36 Amerari anapatsidwa ntchito yosamalira mitengo ya chihema, nsichi zake, mizati yake, matsinde ake, ndi zida zake zonse, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito, Onani mutuwo |