Numeri 28:28 - Buku Lopatulika28 ndi nsembe yake ya efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201428 ndi nsembe yake ya efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa28 Muperekenso chopereka cha chakudya wosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero28 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pazikhala chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri. Onani mutuwo |
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.