Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 28:27 - Buku Lopatulika

27 Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 koma mupereke nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Muzipereka nsembe zopsereza za ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa imodzi yayimuna ndi ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi monga fungo lokomera Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 28:27
6 Mawu Ofanana  

Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;


koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;


Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.


ndi nsembe yake ya efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi,


pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa