Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 28:26 - Buku Lopatulika

26 Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 “Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Chauta, pa tsiku la chikondwerero cha masabata, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 “ ‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 28:26
13 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita.


ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.


Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;


Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.


Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena;


Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi;


Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.


Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choyamba cha iwo akugona.


Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoyamba za zolengedwa zake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa