Numeri 28:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Chauta adauza Mose kuti, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Yehova anawuza Mose kuti, Onani mutuwo |
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.