Numeri 28:2 - Buku Lopatulika2 Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 “Lamula Aisraele, ndipo uŵauze kuti, ‘Muzisamala kupereka kwa Ine pa nthaŵi yake zopereka zanga, chakudya changa cha nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo londikomera.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 “Lamula Aisraeli kuti, ‘Onetsetsani kuti mukupereka kwa Ine pa nthawi yoyikika, chopereka cha chakudya chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Ine.’ Onani mutuwo |
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.