Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 24:9 - Buku Lopatulika

9 Anaunthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Anauthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Adamyata, nagona pansi ngati mkango ngati mkango wamphongo kapena waukazi. Kodi amuutse ndani? Ndi wodala munthu amene aŵadalitsa, ndi wotembereredwa munthu amene aŵatemberera.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi, monga mkango waukazi, adzamuputa ndani? “Amene adalitsa iwe, adalitsike ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:9
21 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.


Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.


Yuda ndi mwana wa mkango, kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera; anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?


Ndipo anaimika mikango khumi ndi iwiri mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko lililonse lina simunapangidwe wotere.


Ndi mpando wachifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi chopondapo mapazi chagolide, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo.


Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamgonjetsa; koma udzagwada pamaso pake.


Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa. Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?


Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu.


Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.


Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe.


Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri la Ziyoni, ndi kuchitunda kwake komwe.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika.


Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.


Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.


Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.


Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.


Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine.


Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;


Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa