Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 24:8 - Buku Lopatulika

8 Mulungu amtulutsa mu Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Mulungu amtulutsa m'Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mulungu adaŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ali ndi mphamvu zonga za njati, adzapha mitundu ya adani ao, adzaswa mafupa ao ndi kuŵaboola ndi mivi yao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto ali ndi mphamvu ngati za njati. Amawononga mitundu yomuwukira ndi kuphwanya mafupa awo, amalasa ndi mivi yake.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:8
18 Mawu Ofanana  

Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.


Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao.


Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu.


Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya. Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.


Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe.


Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.


Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.


Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe.


Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.


Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.


Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.


Mulungu awatulutsa mu Ejipito; mphamvu yake ikunga ya njati.


Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.


nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.


Ndidzawaunjikira zoipa; ndidzawathera mivi yanga.


Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi, ndi lupanga langa lidzalusira nyama; ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa, ndi mutu wachitsitsi wa mdani.


Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;


Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a mu Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka mu Ejipito; ndi chija munachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordani, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa