Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 23:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Tsono adabwerera kwa Balaki, ndipo adangoona akuimirira pafupi ndi nsembe yake yopsereza, ali ndi akalonga a ku Mowabu aja. Balaki adamufunsa kuti, “Nanga Chauta wakuuzani zotani?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 23:17
5 Mawu Ofanana  

pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni.


Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m'kamwa mwake, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti.


Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ukani, Balaki, imvani; ndimvereni, mwana wa Zipori.


Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?


Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa