Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 18:28 - Buku Lopatulika

28 Momwemo inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yochokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israele; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Momwemo inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yochokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israele; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Choncho inunso muzipereka zopereka zanu kwa Chauta, zotapa pa chachikhumi chilichonse chimene mulandira kwa Aisraele. Pa zimene mwalandirazo mutengeko mphatso ya Chauta, ndipo mupatse wansembe Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:28
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.


Ndipo akuyesereninso nsembe yanu yokweza monga tirigu wa padwale, monga mopondera mphesa modzala.


Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake.


Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.


m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa