Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 18:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse mu Israele, likhale cholowa chao, mphotho ya pa ntchito yao alikuichita, ntchito ya chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse m'Israele, likhale cholowa chao, mphotho ya pa ntchito yao alikuichita, ntchito ya chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 “Ndaŵapatsa Alevi chachikhumi chilichonse m'dziko la Israele kuti chikhale chigawo chao, chifukwa cha ntchito imene akuigwira m'chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 “Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:21
26 Mawu Ofanana  

ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.


Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu.


Ndipo Yosefe analamulira lamulo la padziko la Ejipito kufikira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhale la Farao.


Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkulu woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wake ndiye wotsatana naye.


amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake;


ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.


Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma.


Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako.


Ndi Aisraele onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.


Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, kunyumba za chuma.


namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.


Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti chipangano changa chikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu.


Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.


Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.


Sendera nalo kuno fuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire.


Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akutuluka kunkhondo apereke kwa Yehova: munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa.


Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adatuluka m'chuuno cha Abrahamu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa