Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 18:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe cholowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe cholowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Ndipo Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe udzakhala wopanda choloŵa m'dziko mwao, ndiponso udzakhala wopanda gawo lililonse pakati pao. Ine ndine gawo lako ndi choloŵa chako pakati pa Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 18:20
20 Mawu Ofanana  

Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.


Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo.


Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa.


Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.


Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; chifukwa chake ndidzakhulupirira.


Ndipo adzakhala nacho cholowa; Ine ndine cholowa chao; musawapatsa cholandira chao mu Israele; Ine ndine cholandira chao.


Ndipo iwe ndi ana ako aamuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.


Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele.


Chifukwa chake Levi alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi abale ake; Yehova mwini wake ndiye cholowa chake, monga Yehova Mulungu wake ananena naye.


Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.


Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.


ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu ntchito zonse za dzanja lanu muzichitazi.


Koma fuko la Levi sanalipatse cholowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israele, zochitika ndi moto, ndizo cholowa chake, monga Iye adanena naye.


Koma fuko la Levi, Mose analibe kulipatsa cholowa: Yehova Mulungu wa Israele, ndiye cholowa chao, monga ananena nao.


Pakuti Mose adapatsa mafuko awiri, ndi fuko la hafu, cholowa tsidya ilo la Yordani; koma sanapatse Alevi cholowa pakati pao.


Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo cholowa chao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi fuko la Manase logawika pakati adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani kum'mawa, chimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa