Numeri 15:25 - Buku Lopatulika25 Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Wansembe achite mwambo wopepesera machimo a mpingo wonse wa Aisraele ndipo anthuwo adzakhululukidwa, chifukwa choti adalakwa mosadziŵa. Tsono atabwera ndi zopereka zao ngati nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, ndiponso ngati nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta, kuti azimpepesa pa cholakwa chao chija, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo. Onani mutuwo |