Numeri 15:24 - Buku Lopatulika24 pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Ngati cholakwacho chidachitika mosadziŵa, mpingo womwe osazindikira, pamenepo mpingo wonsewo upereke mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Apereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chakumwa, potsata zimene ndidakulamulani. Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa. Onani mutuwo |
Otengedwa ndende, atatuluka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisraele onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, anaankhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.