Numeri 14:14 - Buku Lopatulika14 ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Tsono Aejipito azidzasimbira anthu a m'dziko muno. Iwo amva kale kuti Inu Chauta muli pakati pa anthu ameneŵa. Inu Chauta mumaŵaonekera maso ndi maso, ndipo mtambo wanu umaŵaphimba. Masana mumaŵatsogolera ndi mtambo, usiku mumaŵatsogolera ndi moto. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Ndipo iwowo adzawuza anthu okhala mʼdziko lino zimenezi. Anthuwa amva kale kuti Inu Yehova mumakhala pakati pa anthu amenewa ndi kuti Inuyo Yehova mwawaonekera maso ndi maso. Mtambo wanu umakhala pamwamba pawo ndiponso mumayenda nawo mu mtambo woyima, masana ndi moto woyima, usiku. Onani mutuwo |