Numeri 11:31 - Buku Lopatulika31 Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, n'kudza nazo zinziri zochokera kunyanja, ndipo zidagwa kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201431 Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zochokera kunyanja, nizitula kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa31 Tsono Chauta adautsa mphepo kuchokera ku nyanja. Mphepoyo idabwera ndi zinziri, ndipo zidagwera pafupi ndi mahema. Kuchokera kumahemako, zinzirizo zidagwa pa mtunda woyenda ulendo wa tsiku limodzi mbali imodzi, mbali inanso chimodzimodzi, mozungulira mahemawo. Zitaunjikana, mjintchi wake unali ngati mita limodzi kuchokera pansi mpaka pamwamba. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero31 Pamenepo Yehova anawutsa mphepo yochokera ku nyanja imene inabweretsa zinziri. Zinzirizo zinagwera pansi kuzungulira msasa, mtunda wa kilomita imodzi mbali zonse ndipo msinkhu wake unali mita imodzi. Onani mutuwo |