Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 11:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wake wonse, ndi mawa lake lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa chigono.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wake wonse, ndi mawa lake lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa chigono.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Anthu atadzuka, ankagwira zinzirizo masana onse ndi usiku. M'maŵa mwakenso tsiku lathunthu, adachita chimodzimodzi. Panalibe ndi mmodzi yemwe amene adagwira zinziri zochepera makilogaramu chikwi chimodzi. Ndipo adaziyanika kuzungulira mahema onsewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 11:32
3 Mawu Ofanana  

Koma omeri ndilo limodzi la magawo khumi la efa.


Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri.


Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa