Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.
Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.
Popeza sanatumikire Inu mu ufumu wao, ndi mu ubwino wanu wochuluka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikulu ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerere kuleka ntchito zao zoipa.
chifukwa sanamvere mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.