Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 9:33 - Buku Lopatulika

33 Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwachita zoona, koma ife tachita choipa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwachita zoona, koma ife tachita choipa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Komabe Inu mwakhala olungama pa zonse zimene zatigwera, ndipo mwachita zokhulupirika, koma ife tachita zolakwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Koma Inu mwakhala wolungama pa zonse zimene zakhala zikutichitikira. Mwachita zokhulupirika, koma ife tachita zolakwa.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:33
16 Mawu Ofanana  

Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?


Yehova Mulungu wa Israele, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tili pamaso panu m'kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi.


ndi mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunge chilamulo chanu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawachitira umboni nazo.


ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.


Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindule nako.


Pakuti Mulungu alibe chifukwa cha kulingiriranso za munthu, kuti afike kwa Iye kudzaweruzidwa.


Talakwa pamodzi ndi makolo athu; tachita mphulupulu, tachita choipa.


Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.


Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.


Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide.


Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?


chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.


Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.


ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayende m'malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, koma mwachita monga mwa maweruzo a amitundu okhala pozungulira panu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa