Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 “Nchifukwa chake tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, mumasunga chipangano ndi chikondi chanu chosasinthika. Musalole kuti zosautsa zathu zonse zikuwonekereni ngati zochepa. Zosautsazo zatigwera ife, mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu, ndiponso anthu anu onse, kuyambira nthaŵi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 “Nʼchifukwa chake, tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa kwambiri mumasunga pangano ndi chikondi chosasinthika. Musalole kuti mavuto onse amene atigwera ife, mafumu athu, atsogoleri athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu ndi anthu ena onse kuyambira nthawi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero aoneke ochepa pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:32
42 Mawu Ofanana  

Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu wolingana ndi Inu m'thambo la kumwamba, kapena padziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu,


Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake.


Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.


Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asiriya kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.


Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'mizinda ya Amedi.


Masiku ake Farao Neko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.


Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni.


ndi amitundu otsala amene, Osinapara wamkulu ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m'mizinda ya Samariya, ndi m'dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Yufurate.


anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe chiyambire masiku a Esarahadoni mfumu ya Asiriya, amene anatikweretsa kuno.


Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere;


ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;


Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.


Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.


Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.


Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.


Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.


Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,


sitinamvere atumiki anu aneneri, amene ananena m'dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m'dziko.


Yehova, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani.


Ndipo mukapanda kundimvera, zingakhale izi, ndidzaonjeza kukulangani kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.


Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.


Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zoipa zanu.


Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.


Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu;


ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.


Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.


Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa